Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 7:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma za izi munalembazi; kuli bwino kwa munthu kusakhudza mkazi.

2. Koma cifukwa ca madama munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha.

3. Mwamunayo apereke kwa mkazi mangawa ace; koma modzimodzinso mkazi kwa mwamuna.

4. Mkazi alibe ulamuliro wa pa thupi lace la iye yekha, koma mwamuna ndiye; koma momwemonso mwamuna alibe ulamuliro wa pa thupi laiye yekha, koma mkazi ndiye.

5. Musakanizana, koma ndi kubvomerezana kwanu ndiko, kwa nthawi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, cifukwa ca kusadziletsa kwanu.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 7