Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 5:8-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. cifukwa cace ticita phwando, si ndi cotupitsa cakale, kapena ndi cotupttsaca dumbo, ndi kuipa mtima, koma ndi mkate wosatupa wa kuona mtima, ndi coonadi.

9. Ndinalembera inu m'kalata uja, kuti musayanjane ndi acigololo;

10. si konse konse ndi acigololo a dziko lino lapansi, kapena ndi osirira, ndi okwatula, kapena ndi opembedza mafano; pakuti nkutero mukaturuke m'dziko lapansi;

11. koma tsopano ndalembera inu kuti musayanjane naye, ngati wina wochedwa mbale ali wacigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, iai.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 5