Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 5:7-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Tsukani cotupitsa cakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, monga muli osatupa. Pakutinso Paskha wathu waphedwa, ndiye Kristu;

8. cifukwa cace ticita phwando, si ndi cotupitsa cakale, kapena ndi cotupttsaca dumbo, ndi kuipa mtima, koma ndi mkate wosatupa wa kuona mtima, ndi coonadi.

9. Ndinalembera inu m'kalata uja, kuti musayanjane ndi acigololo;

10. si konse konse ndi acigololo a dziko lino lapansi, kapena ndi osirira, ndi okwatula, kapena ndi opembedza mafano; pakuti nkutero mukaturuke m'dziko lapansi;

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 5