Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 4:9-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu anaoneketsa ife atumwi otsiriza, monga titi tife; pakuti takhala ife coonetsedwa ku dziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu.

10. Tiri opusa ife cifukwa ca Kristu, koma muli ocenjera inu mwa Kristu; tiri ife ofoka, koma inu amphamvu; inu ndinu olemekezeka, koma ife ndife onyozeka.

11. Kufikira nthawi yomwe yino timva njala, timva ludzu, tid amarisece, tikhomedwa, tiribe pokhazikika;

12. ndipo tigwiritsa nchito, ndi kucita ndi manja athu a ife tokha; polalatidwa tidalitsa; pozunzidwa, tipirira;

13. ponamizidwa, tipempha; takhala monga zonyansa za dziko lapansi, litsiro la zinthu zonse, kufikira tsopano,

14. Sindilembera izi kukucititsani manyazi, koma kucenjeza inu monga ana anga okondedwa.

15. Pakuti mungakhale muli nao aphunzitsi zikwi khumi mwa Kristu, mulibe atate ambiri; pakuti mwa Kristu Yesu ine ndinabala Inu mwa Uthenga Wabwino.

16. Cifukwa cace ndikupemphani, khalani akutsanza ine.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 4