Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 4:12-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. ndipo tigwiritsa nchito, ndi kucita ndi manja athu a ife tokha; polalatidwa tidalitsa; pozunzidwa, tipirira;

13. ponamizidwa, tipempha; takhala monga zonyansa za dziko lapansi, litsiro la zinthu zonse, kufikira tsopano,

14. Sindilembera izi kukucititsani manyazi, koma kucenjeza inu monga ana anga okondedwa.

15. Pakuti mungakhale muli nao aphunzitsi zikwi khumi mwa Kristu, mulibe atate ambiri; pakuti mwa Kristu Yesu ine ndinabala Inu mwa Uthenga Wabwino.

16. Cifukwa cace ndikupemphani, khalani akutsanza ine.

17. Cifukwa ca ici ndatuma kwa inu Timoteo, ndiye mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye, amene adzakumbutsa inu njira zanga za mwa Kristu, monga ndiphunzitsa ponsepom'Mipingo yonse.

18. Koma ena adzitukumula, monga ngati sindinalinkudza kwa inu.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 4