Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 2:11-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Pakuti ndani wa anthu adziwa za munthu, koma mzimu wa munthuyu uli mwa iye? momwemonso za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu wa Mulungu.

12. Koma sitinalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma Mzimu wa kwa Mulungu, kuti tikadziwe zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwaufulu.

13. Zimenenso tilankhula, si ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za munthu, koma ophunzitsidwa ndi Mzimu; ndi kulinganiza zamzimu ndi zamzimu.

14. Koma munthu wa cibadwidwe ca umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sakhoza kuzizindikira, cifukwa ziyesedwa mwauzimu.

15. Koma iye amene ali wauzimu ayesa zonse, koma iye yekha sayesedwa ndi mmodzi yense.

16. Pakuti wadziwa ndani mtima wa Ambuye, kuti akamlangize iye? Koma ife tiri nao mtima wa Kristu.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 2