Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 15:20-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Koma tsopano Kristu waukitsidwa kwa akufa, cipatso coundukula ca iwo akugona.

21. Pakuti monga imfa inadza mwa munthu, kuuka kwa akufa kunadzanso mwa munthu.

22. Pakuti mongamwa Adamu onse amwalira, coteronso mwa Kristu onse akhalitsidwa ndi moyo.

23. Koma yense m'dongosolo lace la iye yekha, cipatso coundukula Kristu, pomwepo iwo a Kristu, pa kubwera kwace.

24. Pomwepo pali cimariziro, pamene adzapereka ufumu kwa Mulungu, ndiye Atate, atatha kuthera ciweruzo conse, ndi ulamuliro wonse, ndi mphamvu yomwe.

25. Pakuti ayenera kucita ufumu kufikira ataika adani onse pansi pa mapazi ace.

26. Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.

27. Pakuti Iye anagonjetsa zonse pansi pa mapazi ace. Koma pamene anena kutizonse zagonjetsedwa, kuzindikirika kuti sawerengapo Iye amene anagonjetsa zonsezo kwa Iye.

28. Ndipo pamene zonsezo: zagonjetsedwa kwa iye, pomwepo Mwana yemwe adzagonjetsedwa kwa iye amene anamgonjetsera zinthuzonse; kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.

29. Ngati si kutero, adzacita ciani iwo amene abatizidwa cifukwa ca akufa? Ngatiakufa saukitsidwa konse, abatizidwa cifukwa ninji cifukwa ca iwo?

30. Nanga 1 ifenso tiri m'moopsya bwanji nthawi zonse?

31. 2 Ndifa tsiku ndi tsiku, ndilumbira pa kudzitamandira kwa inu, abale, kumene ndiri nako mwa Kristu Yesu, Ambuye wathu.

32. 3 Ngati odinalimbana ndi zirombo ku Efeso monga mwa munthu, ndipindulanji? Ngati akufa saukitsidwa, 4 tidye timwepakuti mawa timwalira.

33. Musanyengedwe; 5 mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma

34. 6 Ukani molungama, ndipo musacimwe; pakuti enaalibe cidziwitso ca Mulungu, Ndilankhula kunyaza inu.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 15