Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 14:23-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Cifukwa cace, ngati Mpingo wonse akasonkhane pamodzi, ndi onse akalankhule malilime, ndipo akalowemo anthu osaphunzira kapena osakhulupira, kodi sadzanena kuti mwayaruka?

24. Koma ngati onse anenera, ndipo alowamo wina wosakhulupirira kapena wosaphunzira, atsutsidwa ndi onse; aweruzidwa ndi onse;

25. zobisika za mtima wace zionetsedwa; ndipo cotero adzagwa nkhope yace pansi, nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa inu.

26. Nanga ciani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salmo, ali naco ciphunzitso, ali nalo bvumbulutso, ali nalo lilime, ali naco cimasuliro. Mucite zonse kukumangirira.

27. Ngati wina alankhula lilime, acite ndi awiri, koma oposa atatu iai, ndipo motsatana; ndipo mmodzi amasulire.

28. Koma ngati palibe womasulira, akhale cete mu Mpingo, koma alankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu.

29. Ndipo aneneri alankhule awiri kapena atatu, ndi ena azindikire.

30. Koma ngati kanthu kabvumbulutsidwa kwa wina wakukhalapo, akhale cete woyambayo.

31. Pakuti mukhoza nonse kunenera mmodzi mmodzi, kuti onse aphunzire, ndi onse afulumidwe;

32. ndipo mizimu ya aneneri imvera aneneri;

33. pakuti Mulungu sali Mulungu wa cisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 14