Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 14:11-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Cifukwa cace, ngati sindidziwa mphamvu ya mauwo ndidzakhala kwa iye wolankhulayo wakunja, ndipo wolankhulayo adzakhala wakunja kwaine.

12. Momwemo inunso, popeza muli ofunits its a mphatso zauzimu, funani kuti mukacuruke kukumangirira kwa Mpingo,

13. Cifukwa cace wolankhula lilime, apemphere kuti amasule.

14. Pakuti ngati ndipemphera m'lilime, mzimu wanga upemphera, koma cidziwitso canga cikhala cosabala kanthu.

15. Kuli ciani tsono? Ndidzapemphera ndi mzimu, koma ndidzapempheranso ndi cidziwitso canga; ndidzayimba ndi mzimu, koma ndidzayimbanso ndi cidziwitso.

16. Cifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala wosaphunzira adzati Amen bwanji, pa kuyamika kwako, popeza sadziwa cimene unena?

17. Pakutitu iwe uyamika bwino, koma winayo samangiriridwa.

18. Ndiyanillca Mulungu kuti ndilankhula malilime koposa inu nonse;

19. koma mu Mpingo ndifuna kulankhula mau asanu ndi cidziwitso canga, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula mau zikwi m'lilime.

20. Abale, musakhale ana m'cidziwitso, koma m'coipa khalani makanda, koma m'cidziwitso akulu misinkhu.

21. Kwalembedwa m'cilamulo, Ndi anthu amalilime ena ndipo ndi milomo yina ndidzalankhula nao anthu awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye.

22. Cotero malilime akhala ngati cizindikilo, si kwa iwo akukhulupira, koma kwa iwo osakhulupira; koma kunenera sikuli kwa iwo osakhulupira, koma kwa two amene akhulupira.

23. Cifukwa cace, ngati Mpingo wonse akasonkhane pamodzi, ndi onse akalankhule malilime, ndipo akalowemo anthu osaphunzira kapena osakhulupira, kodi sadzanena kuti mwayaruka?

24. Koma ngati onse anenera, ndipo alowamo wina wosakhulupirira kapena wosaphunzira, atsutsidwa ndi onse; aweruzidwa ndi onse;

25. zobisika za mtima wace zionetsedwa; ndipo cotero adzagwa nkhope yace pansi, nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa inu.

26. Nanga ciani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salmo, ali naco ciphunzitso, ali nalo bvumbulutso, ali nalo lilime, ali naco cimasuliro. Mucite zonse kukumangirira.

27. Ngati wina alankhula lilime, acite ndi awiri, koma oposa atatu iai, ndipo motsatana; ndipo mmodzi amasulire.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 14