Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 12:9-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. kwa wina cikhulupiriro, mwa Mzimu yemweyo; ndi kwa wina mphatso za maciritso, mwa Mzimu mmodziyo;

10. ndi kwa wina macitidwe a mphamvu; ndi kwa wina cinenero; ndi kwa wina cizindikiro ca mizimu; kwa wina malilime a mitundu mitundu; ndi kwa wina mamasulidwe a malilime.

11. Koma zonse izi acita Mzimu mmodzi yemweyo, nagawira yense payekha monga afuna.

12. Pakuti monga thupi liri limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri; koma ziwalo zonse za thupilo, pokhala zambiri, ziri thupi limodzi; momwemonso Kristu.

13. Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse rinabatizidwa kulowa m'thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Ahelene, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa Mzimu mmodzi.

14. Pakutinso thupisilikhala ciwalo cimodzi, koma zambiri.

15. Ngati phazi likati, Popeza sindiri dzanja, sindiri wa thupi; kodi siliri la thupi cifukwa ca ici?

16. Ndipo ngati khutu likati, Popeza sindiri diso, sindiri wa thupi; kodi siliri la thupi cifukwa ca ici?

17. Ngati thupi lonse likadakhala diso, kukadakhala kuti kununkhiza?

18. Koma tsopano, Mulungu anaika ziwalo zonsezo m'thupi, monga anafuna.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 12