Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 12:4-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo pali mphatso zosiyana, koma Mzimu yemweyo.

5. Ndipo pali mautumiki osiyana, koma Ambuye yemweyo.

6. Ndipo pali macitidwe osiyana, koma Mulungu yemweyo, wakucita zinthu zonse mwa onse.

7. Koma kwa yense kwapatsidwa maonekedwe a Mzimu kuti apindule nao.

8. Pakuti kwa mmodzi kwapatsidwa mwa Mzimu mau a nzeru; koma kwa mnzace mau a cidziwitso, monga mwa Mzimu yemweyo:

9. kwa wina cikhulupiriro, mwa Mzimu yemweyo; ndi kwa wina mphatso za maciritso, mwa Mzimu mmodziyo;

10. ndi kwa wina macitidwe a mphamvu; ndi kwa wina cinenero; ndi kwa wina cizindikiro ca mizimu; kwa wina malilime a mitundu mitundu; ndi kwa wina mamasulidwe a malilime.

11. Koma zonse izi acita Mzimu mmodzi yemweyo, nagawira yense payekha monga afuna.

12. Pakuti monga thupi liri limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri; koma ziwalo zonse za thupilo, pokhala zambiri, ziri thupi limodzi; momwemonso Kristu.

13. Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse rinabatizidwa kulowa m'thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Ahelene, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa Mzimu mmodzi.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 12