Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 12:1-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma za mphatso zauzimu, abale, sindifuna kuti mukhale osadziwa.

2. Mudziwa kuti pamene munali amitundu, munatengedwa kunka kwa mafano aja osalankhula, monga munatsogozedwa.

3. Cifukwa cace ndikuuzani inu, kuti palibe munthu wakulankhula mwa Mzimu wa Mulungu, anena, Yesu ngwotembereredwa; ndipo palibe wina akhoza kunena, Yew ali Ambuye, koma mwa Mzimu Woyera.

4. Ndipo pali mphatso zosiyana, koma Mzimu yemweyo.

5. Ndipo pali mautumiki osiyana, koma Ambuye yemweyo.

6. Ndipo pali macitidwe osiyana, koma Mulungu yemweyo, wakucita zinthu zonse mwa onse.

7. Koma kwa yense kwapatsidwa maonekedwe a Mzimu kuti apindule nao.

8. Pakuti kwa mmodzi kwapatsidwa mwa Mzimu mau a nzeru; koma kwa mnzace mau a cidziwitso, monga mwa Mzimu yemweyo:

9. kwa wina cikhulupiriro, mwa Mzimu yemweyo; ndi kwa wina mphatso za maciritso, mwa Mzimu mmodziyo;

10. ndi kwa wina macitidwe a mphamvu; ndi kwa wina cinenero; ndi kwa wina cizindikiro ca mizimu; kwa wina malilime a mitundu mitundu; ndi kwa wina mamasulidwe a malilime.

11. Koma zonse izi acita Mzimu mmodzi yemweyo, nagawira yense payekha monga afuna.

12. Pakuti monga thupi liri limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri; koma ziwalo zonse za thupilo, pokhala zambiri, ziri thupi limodzi; momwemonso Kristu.

13. Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse rinabatizidwa kulowa m'thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Ahelene, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa Mzimu mmodzi.

14. Pakutinso thupisilikhala ciwalo cimodzi, koma zambiri.

15. Ngati phazi likati, Popeza sindiri dzanja, sindiri wa thupi; kodi siliri la thupi cifukwa ca ici?

16. Ndipo ngati khutu likati, Popeza sindiri diso, sindiri wa thupi; kodi siliri la thupi cifukwa ca ici?

17. Ngati thupi lonse likadakhala diso, kukadakhala kuti kununkhiza?

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 12