Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 11:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Khalani onditsanza ine, monga inenso oditsanza Kristu.

2. Ndipo ndikutamandani kuti m'zinthu zonse mukumbukila ine, ndi kuti musunga miyambo monga ndinapereka kwa inu.

3. Koma ndifunakuti mudziwe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Kristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Kristu ndiye Mulungu,

4. Mwamuna yense wobveka mutu, popemphera kapena ponenera, anyoza mutu wace.

5. Koma mkazi yense wakupemphera, kapena kunenera, wobvula mutu, anyoza mutu wace; pakuti kuli cimodzimodzi kumetedwa.

6. Pakuti ngati mkazi sapfunda, asengedwenso; koma ngati kusengedwa kapena kumetedwa kucititsa manyazi, apfunde,

7. Pakuti mwamuna sayenera kubvala pamutu, popeza akhala fanizo ndi ulemerero wa Mulungu: koma mkazi ali ulemerero wa mwamuna.

8. Pakuti mwamuna sakhala wa kwa mkazi; koma mkazi wa kwa mwamuna;

9. pakutinso mwamuna sanalengedwa cifukwa ca mkazi;

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 11