Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 10:11-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Koma izi zinacitika kwa iwowa monga zoticenjeza, ndipo zinalembedwa kuticenjeza ife, amene matsirizidwe a nthawi ya pansi pano adafika pa ife.

12. Cifukwa cace iyewakuyesa kuti ali ciriri, ayang'anire kuti angagwe,

13. Sicinakugwerani inu ciyeso koma ca umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi ciyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.

14. Cifukwa cace, okondedwa anga, thawani kupembedza mafano.

15. Ndinena monga kwa anzeru; lingirirani inu cimene ndinena.

16. Cikho ca dalitso cimene tidalitsa, siciri ciyanjano ca mwazi wa Kristu kodi? Mkate umene tinyema suli ciyanjano ca thupi la Kristu kodi?

17. Pakuti mkate ndiwo umodzi, cotero ife ambiri ndife thupi limodzi; pakuti ife tonse titengako ku mkate umodzi.

18. Tapenyani Israyeli monga mwa thupi; kodi iwo akudya nsembezo alibe ciyanjano ndi guwa la nsembe?

19. Ndinena ciani tsono? kuti coperekedwa nsembe kwa mafano ciri kanthu? Kapena kuti fane liri kanthu kodi?

20. Koma nditi kuti zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda; ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 10