Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 1:21-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Pakuti popeza m'nzeru ya Mulungu dziko lapansi, mwa nzeru yace, silinadziwa Mulungu, cidamkonda Mulungu kupulumutsa okhulupirawo mwa copusa ca kulalikira.

22. Ndipo popeza Ayuda afunsa zizindikilo, ndi Ahelene atsata nzeru:

23. koma ife tilalikira Kristu wopacikidwa, kwa Ayudatu cokhumudwitsa, ndi kwa amitundu cinthu copusa;

24. koma kwa iwo oitanidwa, ndiwo Ayuda ndi Ahelene, Kristu 1 mphamvu ya Mulungu, ndi 2 nzeru ya Mulungu.

25. Cifukwa kuti copusa ca Mulungu ciposa anthu ndi nzeru zao; ndipo cofoka ca Mulunguciposa anthu ndi mphamvu yao.

26. Pakuti penyani maitanidwe anu, abale, kuti 3 saitanidwa ambiri anzeru, monga mwa thupi; ambiri amphamvu, mfulu zambiri, iai;

27. koma 4 Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi, kuti akacititse manyazi anzeru; ndipo zofoka za dziko lapansi Mulungu anazisankhula, kuti akacititse manyazi zamphamvu;

28. ndipo zopanda pace za dziko lapansi, ndi zonyozeka, anazisankhula Mulungu, ndi zinthu zoti kulibe; 5 kuti akathere zinthu zoti ziriko;

29. 6 kuti thupi liri lonse lisadzitamande pamaso pa Mulungu.

30. Koma kwa iye muli inu mwa Kristu Yesu, 7 amene anayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi cilungamo ndi ciyeretso ndi ciombolo;

31. kuti monga mwalembedwa, iye amene adzitamanda, adzitamande mwa Ambuye.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 1