Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 7:4-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo mau a Yehova wa makamu anadza kwa ine, ndi kuti,

5. Nena kwa anthu onse a m'dziko, ndi kwa ansembe, kuti, Muja mukasala ndi kulira mwezi wacisanu, ndi wacisanu ndi citatu, zaka izi makumi asanu ndi awiri, kodi mukasalira Ine, Inedi?

6. Ndipo pamene mukadya, ndi pamene mukamwa, mukadya si ndinu, mukamwa si ndinu kodi?

7. Si ndiwo mau Yehova anawalalikira mwa aneneri oyamba aja, muja Yerusalemu anali nao okhalamo, ndi wokhazikika; ndi m'midzi mwace pozungulira pace, ndi m'dziko la kumwela, ndi m'cidikha munali anthu okhalamo?

8. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Zekariya, ndi kuti,

9. Watero Yehova wa makamu, kuti, Weruzani ciweruzo coona, nimucitire yense mnzace cifundo ndi ukoma mtima;

10. musazunza mkazi wamasiye, kapena ana amasiye, mlendo kapena waumphawi; ndipo nnena mmodzi wa inu alingirire m'mtima mwace kumcitira coipa munthu mnzace.

11. Koma anakana kumvera, nakaniza phewa lao, natseka makutu ao, kuti asamve.

12. Inde, anasanduliza mitima yao ikhale ngati mwala woti gwa, kuti angamve cilamulo, ndi mau amene Yehova wa makamu anatumiza ndi Mzimu wace mwa aneneri oyamba aja; m'menemo munafuma mkwiyo waukuru wocokera kwa Yehova wa makamu.

Werengani mutu wathunthu Zekariya 7