Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 6:13-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. inde adzamanga Kacisi wa Yehova; nadzasenza ulemererowo, nadzakhala ndi kulamulira pa mpando wacifumu wace; nadzakhala wansembe pampando wacifumu wace; ndi uphungu wa mtendere udzakhala pakati pa iwo awiri,

14. Ndipo akorona adzakhala wa Kelemu, ndi wa Tobiya, ndi wa Yedaya, ndi wa Keni mwana wa Zefaniya, akhale cikumbutso m'Kacisi wa Yehova.

15. Ndipo iwo akukhala kutari adzafika, nadzamanga ku Kacisi wa Yehova, ndipo inu mudzadziwa kuti Yehova wa makamu ananditumiza kwa inu. Ndipo ici cidzacitika ngati mudzamvera mwacangu mau a Yehova Mulungu wanu.

Werengani mutu wathunthu Zekariya 6