Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 4:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo mthengayo adalankhula nane, anadzanso, nandiutsa ngati munthu woutsidwa m'tulo tace.

2. Ndipo anati kwa ine, Uona ciani? Ndipo ndinati, Ndaona, taonani, coikapo nyali ca golidi yekha yekha, ndi mbale yace pamwamba pace, ndi nyali zace zisanu ndi ziwiri pamenepo; nyalizo zinali ndi misiwe isanu ndi iwiri, ndiyo ya nyalizo zinali pamwamba pace;

3. ndi mitengo iwiri yaazitona pomwepo, wina ku dzanja lamanja la mbaleyo, ndi wina ku dzanja lace lamanzere.

4. Ndipo ndinayankha ndi kunena ndi mthenga wakulankhula ndi ine, ndi kuti, Izi nziani mbuyanga?

5. Ndipo mthenga wakulankhula ndi ine anayankha, nati kwa ine, Sudziwa kodi kuti nziani izi? Ndipo ndinati, Iai, mbuyanga.

6. Pamenepo anayankha, nanena kwa ine, ndi kuti, Awa ndi mau a Yehova kwa Zerubabele, Ndi khamu la nkhondo ai, ndi mphamvu ai, koma ndi Mzimu wanga, ati Yehova wa makamu.

7. Ndiwe yani, phiri lalikuru iwe? pamaso pa Zerubabele udzasanduka cidikha; ndipo adzaturutsa mwala wa cimbudzi, ndi kupfuula, Cisomo, cisomo nao.

8. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, ndi kuti,

Werengani mutu wathunthu Zekariya 4