Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 4:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo mthengayo adalankhula nane, anadzanso, nandiutsa ngati munthu woutsidwa m'tulo tace.

2. Ndipo anati kwa ine, Uona ciani? Ndipo ndinati, Ndaona, taonani, coikapo nyali ca golidi yekha yekha, ndi mbale yace pamwamba pace, ndi nyali zace zisanu ndi ziwiri pamenepo; nyalizo zinali ndi misiwe isanu ndi iwiri, ndiyo ya nyalizo zinali pamwamba pace;

3. ndi mitengo iwiri yaazitona pomwepo, wina ku dzanja lamanja la mbaleyo, ndi wina ku dzanja lace lamanzere.

4. Ndipo ndinayankha ndi kunena ndi mthenga wakulankhula ndi ine, ndi kuti, Izi nziani mbuyanga?

5. Ndipo mthenga wakulankhula ndi ine anayankha, nati kwa ine, Sudziwa kodi kuti nziani izi? Ndipo ndinati, Iai, mbuyanga.

Werengani mutu wathunthu Zekariya 4