Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 3:6-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo mthenga wa Yehova anamcitira Yoswa umboni, ndi kuti,

7. Atero Yehova wa makamu: Ukadzayenda m'njira zanga, ndi kusunga udikiro wanga, pamenepo udzaweruza nyumba yanga, ndi kusunga mabwalo anga, ndipo ndidzakupatsa malo oyendamo mwa awa oimirirapo.

8. Tamvera tsono, Yoswa mkulu wa ansembe, iwe ndi anzako akukhala pansi pamaso pako; pakuti iwo ndiwo cizindikilo; pakuti taonani, ndidzafikitsa mtumiki wanga, ndiye Mphukira.

9. Pakuti taona, mwalawo ndinauika pamaso pa Yoswa; pa mwala umodzi pali maso asanu ndi awiri; taonani, ndidzaloca malocedwe ace, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzacotsa mphulupulu ya dziko lija tsiku limodzi.

10. Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, mudzaitanizana yense mnansi wace patsinde pa mpesa ndi patsinde pa mkuyu.

Werengani mutu wathunthu Zekariya 3