Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 2:3-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo taonani, mthenga wolankhula nane anaturuka, ndi mthenga wina anaturuka kukomana naye,

4. nanena naye, Thamanga, lankhula ndi mnyamata uyu, ndi kuti, M'Yerusalemu mudzakhala anthu ngati m'midzi yopanda malinga, cifukwa ca kucuruka anthu ndi zoweta momwemo.

5. Pakuti Ine, ati Yehova, ndidzakhala kwa iye linga lamoto pozungulira pace, ndipo ndidzakhala ulemerero m'kati mwace.

6. Haya, haya, thawani ku dziko la kumpoto, ati Yehova; pakuti ndinakubalalitsani ngati mphepo zinai za kuthambo, ati Yehova.

Werengani mutu wathunthu Zekariya 2