Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 2:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, munthu ndi cingwe coyesera m'dzanja lace.

2. Ndipo ndinati, Upita kuti? Ndipo anati kwa ine, Kukayesa Yerusalemu, kuona ngati citando cace ncotani, ndi m'litali mwace motani.

3. Ndipo taonani, mthenga wolankhula nane anaturuka, ndi mthenga wina anaturuka kukomana naye,

4. nanena naye, Thamanga, lankhula ndi mnyamata uyu, ndi kuti, M'Yerusalemu mudzakhala anthu ngati m'midzi yopanda malinga, cifukwa ca kucuruka anthu ndi zoweta momwemo.

5. Pakuti Ine, ati Yehova, ndidzakhala kwa iye linga lamoto pozungulira pace, ndipo ndidzakhala ulemerero m'kati mwace.

Werengani mutu wathunthu Zekariya 2