Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 14:4-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndi mapazi ace adzaponda tsiku lomwelo pa phiri la Azitona, liri pandunji pa Yerusalemu kum'mawa, ndi phiri la Azitona lidzang'ambika pakati kuloza kum'mawa ndi kumadzulo, ndipo padzakhala cigwa cacikuru; ndi gawo lina la phirilo lidzamuka kumpoto, ndi gawo lina kumwela.

5. Pamenepo mudzathawa kudzera cigwa ca mapiri anga; pakuti cigwa ca mapiri cidzafikira ku Azali; ndipo mudzathawa monga umo munathawira cibvomezi, masiku a Uziya mfumu ya Yuda; ndipo Yehova Mulungu wanga adzadza, ndi opatulika onse pamodzi ndi Inu.

6. Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo, sikudzakhala kuunika, zowalazo zidzada;

7. koma lidzakhala tsiku la pa lokha lodziwika ndi Yehova; palibe usana, palibe usiku; koma kudzatero kuti madzulo kudzati mbe.

8. Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo kuti madzi amoyo adzaturuka ku Yerusalemu; gawo lao lina kumka ku nyanja ya kum'mawa, ndi gawo lina kumka ku nyanja ya kumadzulo; adzatero nyengo ya dzinja ndi ya mwamvu.

Werengani mutu wathunthu Zekariya 14