Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 13:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tsiku lomwelo padzatsegukira nyumba ya Davide ndi okhala m'Yerusalemu kasupe wa kwa ucimo ndi cidetso.

2. Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzaononga maina a mafano m'dziko; ndipo sadzakumbukikanso; ndipo ndidzacotsa m'dziko aneneri ndi mzimu wacidetso.

3. Ndipo kudzacitika, akaneneranso wina, atate wace ndi mai wace ombala adzanena naye, Sudzakhala ndi moyo, pakuti unena bodza m'dzina la Yehova; ndipo atate wace ndi mai wace ombala adzamgwaza ponenera iye.

4. Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo kuti aneneri adzacita manyazi yense ndi masomphenya ace, ponenera iye; ndipo sadzabvala copfunda caubweya kunyenga naco;

5. koma adzati, Sindiri mneneri, ndiri wolima munda; pakuti munthu anandiyesa kapolo kuyambira ubwana wanga.

6. Ndipo wina akati kwa iye, Zipsera izi m'manja mwako nza ciani? adzayankha, Ndizo za mabala anandilasa m'nyumba ya ondikonda.

Werengani mutu wathunthu Zekariya 13