1. Tsegula pa makomo ako Lebano, kuti moto uthe mikungudza yako.
2. Cema, mtengo wamlombwa, pakuti mkungudza wagwa, popeza mitengo yokoma yaipitsidwa; cemani athundu a ku Basani, pakuti nkhalango yocinjirizika yagwa pansi.
3. Mau a kucema kwa abusa! pakuti ulemerero wao waipsidwa; mau a kubangula kwa misona ya mikango! pakuti kudzikuza kwa Yordano kwaipsidwa.
4. Atero Yehova Mulungu wanga: Dyetsani zoweta zakukaphedwa;
5. zimene eni ace azipha, nadziyesera osaparamula; ndi iwo akuwagulitsa akuti, Alemekezedwe Yehova, pakuti ine ndine wolemera; ndi abusa ao sazicitira cifundo.
6. Pakuti sindidzacitiranso cifundo okhala m'dzikomo, ati Yehova; koma taonani, ndidzapereka anthu, yense m'dzanja la mnansi wace, ndi m'dzanja la mfumu yace; ndipo iwo adzakantha dzikoli, ndi m'dzanja mwao sindidzawalanditsa.
7. M'mwemo ndinadyetsa zoweta zakukaphedwa, ndizo zoweta zonyankhalala. Ndipo ndinadzitengera ndodo ziwiri; yina ndinaicha Cisomo, inzace ndinaicha Comanganitsa; ndipo ndinadyetsa zowetazo.
8. Ndipo ndinatha abusa atatuwo mwezi umodzi; pakuti mtima wanga unalema nao, ndi mtima waonso unaipidwa nane.
9. Pamenepo ndinati, Sindidzadyetsanso inu; cirikufa cife; cosoweka cisoweke; ndi zotsala zidyane, conse nyama ya cinzace.
10. Ndipo ndinatenga ndodo yanga Cisomo, ndi kuidula pakati, kuti ndiphwanye pangano langa ndinalicita ndi mitundu yonse ya anthu.