Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 10:9-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo ndidzawafesa mwa mitundu ya anthu, ndipo adzandikumbukila m'maiko akutali; nadzakhala pamodzi ndi ana ao, nadzabwera.

10. Ndidzawatenganso ku dziko la Aigupto, ndi kuwasonkhanitsa m'Asuri; ndipo ndidzalowa nao m'dziko la Gileadi ndi Lebano; koma sadzawafikira.

11. Ndipo adzapita pakati pa nyanja ya nsautso, nadzapanda mafunde a m'nyanja, ndi maiwe onse a mtsinje adzaphwa; ndi kudzikuza kwa Asuri kudzagwetsedwa; ndi ndodo yacifumu ya Aigupto idzacoka.

12. Ndipo ndidzawalimbitsa mwa Yehova; ndipo adzayendayendam'dzina lace, ati Yehova.

Werengani mutu wathunthu Zekariya 10