5. Ndipo adzakhala ngati ngwazi zakupondereza adani m'thope la kubwalo kunkhondo; ndipo adzacita nkhondo, cifukwa Yehova ali nao; ndi apakavalo adzacitidwa manyazi.
6. Ndipo ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda, ndi kusunga nyumba ya Yosefe, ndipo ndidzawakhalitsa, pakuti ndawacitira cifundo; ndipo adzakhala monga ngati sindinawataya konse; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, ndipo ndidzawamvera.
7. Ndipo iwo a ku Efraimu adzakhala ngati ngwazi, ndi mtima wao udzakondwera ngati ndi vinyo; ndipo ana ao adzaciona nadzakondwera; mtima wao udzakondwerera mwa Yehova.
8. Ndidzawayimbira mluzu ndi kuwasonkhanitsa, pakuti ndawaombola; ndipo adzacuruka monga anacurukira kale.
9. Ndipo ndidzawafesa mwa mitundu ya anthu, ndipo adzandikumbukila m'maiko akutali; nadzakhala pamodzi ndi ana ao, nadzabwera.
10. Ndidzawatenganso ku dziko la Aigupto, ndi kuwasonkhanitsa m'Asuri; ndipo ndidzalowa nao m'dziko la Gileadi ndi Lebano; koma sadzawafikira.
11. Ndipo adzapita pakati pa nyanja ya nsautso, nadzapanda mafunde a m'nyanja, ndi maiwe onse a mtsinje adzaphwa; ndi kudzikuza kwa Asuri kudzagwetsedwa; ndi ndodo yacifumu ya Aigupto idzacoka.
12. Ndipo ndidzawalimbitsa mwa Yehova; ndipo adzayendayendam'dzina lace, ati Yehova.