Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zefaniya 1:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. MAU a Yehova amene anadza kwa Zefaniya mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya, masiku a Yosiya, mwana wa Amoni mfumu ya Yuda.

2. Kuzitha ndidzazitha zonse kuzicotsa panthaka, ati Yehova.

3. Ndidzatha munthu ndi nyama; ndidzatha mbalame za m'mlengalenga, ndi nsomba za m'nyanja, ndi zokhumudwitsa pamodzi ndi oipa; ndipo ndidzaononga anthu kuwacotsa panthaka, ati Yehova.

4. Ndipo ndidzatambasulira dzanja langa pa Yuda, ndi pa onse okhala m'Yerusalemu; ndipo a ndidzaononga otsala a Baala kuwacotsa m'malo muno, ndi dzina la Akemari pamodzi ndi ansembe;

5. ndi iwo akulambira khamu la kumwamba pamwamba pa matsindwi; ndi iwo akulambira, akulumbira pali Yehova, nalumbiranso pali mfumu;

6. ndi iwo akubwerera osamtsata Yehova; ndi osamfuna Yehova, kapena kufunsira kwa Iye.

7. Khala cete pamaso pa Ambuye Yehova; pakuti tsiku la Yehova liyandikira; pakuti Yehova wakonzeratu nsembe, anapatula oitanidwa ace.

8. Ndipo kudzacitika tsiku la nsembe ya Yehova, kuti ndidzalanga akalonga ndi ana a mfumu, ndi onse akubvala cobvala cacilendo.

Werengani mutu wathunthu Zefaniya 1