Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoweli 2:28-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Ndipo kudzacitika m'tsogolo mwace, ndidzatsanulira mzimu wanga pa anthu onse, ndi ana anu amuna ndi akazi adzanenera, akulu akulu anu adzalota maloto, anyamata anu adzaona masomphenya;

29. ndi pa akapolo ndi adzakazi omwe ndidzatsanulira mzimu wanga masiku awo.

30. Ndipo ndidzaonetsa zodabwiza kuthambo ndi pa dziko lapansi, mwazi, ndi moto, ndi utsi tolo.

31. Dzuwa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Yehova lalikuru ndi loopsa.

Werengani mutu wathunthu Yoweli 2