Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoweli 2:12-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Koma ngakhale tsopano, ati Yehova, munditembenukire Ine ndi mtima wanu wonse, ndi kusala, ndi kulira, ndi kucita maliro;

13. ndipo ng'ambani mitima yanu, si zobvala zanu ai; ndi kurembenukira kwa Yehova Mulungu wanu; pakuti Iye ndiye wacisomo, ndi wodzala cifundo, wosapsa mtima msanga, ndi wocuruka kukoma mtima, ndi woleka coipaco.

14. Kaya, kapena adzabwerera, nadzalekerera, ndi kusiya mdalitso pambuyo pace, ndiwo nsembe yaufa ndi nsembe yathira ya Yehova Mulungu wanu.

15. Ombani lipenga m'Ziyoni, patulani tsiku losala, lalikirani msonkhano woletsa,

16. sonkhanitsani anthu, patulani msonkhano, memezani akulu akulu, sonkhanitsani ana ndi oyamwa mawere; mkwati aturuke m'cipinda mwace, ndi mkwatibwi m'mogona mwace.

17. Ansembe, atumiki a Yehova, alire pakati pa khonde la pakhomo ndi guwa la nsembe, nanene, Alekeni anthu anu, Yehova, musapereka colowa canu acitonze, kuti amitundu awalamulire; adzaneneranji mwa anthu, Ali kuti Mulunguwao?

18. Pamenepo Yehova anacitira dziko lace nsanje, nacitira anthu ace cifundo.

19. Ndipo Yehova anayankha, nati kwa anthu ace, Taonani, ndidzakutumizirani tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; ndipo mudzakhuta ndi izo; ndipo sindidzakuperekaninso mukhale citonzo mwa amitundu;

20. koma ndidzakucotserani kutali nkhondo ya kumpoto, ndi kulingira ku dziko louma ndi lopasuka, a kumaso kwace ku nyanja ya kum'mawa, ndi a kumbuyo kwace ku nyanja ya kumadzulo; ndi kununkha kwace kudzakwera, ndi pfungo lace loipa lidzakwera; pakuti inacita zazikuru.

21. Usaopa, dziko iwe; kondwera, nusekerere; pakuti Yehova wacita zazikuru.

Werengani mutu wathunthu Yoweli 2