Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoweli 1:5-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Galamukani, oledzera inu, nimulire; bumani, nonse akumwa vinyo, cifukwa ca vinyo watsopano; pakuti waletsedwa pakamwa panu.

6. Pakuti mtundu wadza, wakwerera dziko langa, wamphamvu wosawerengeka, mano ace akunga mano a mkango, nukhala nao mano acibwano a mkango waukuru.

7. Unaonongadi mpesa wanga, nunyenya mkuyu wanga, nuukungudza konse, nuutaya; nthambi zace zasanduka zotumbuluka.

8. Lirani ngati namwali wodzimangira m'cuuno ciguduli, cifukwa ca mwamuna wa unamwali wace.

9. Nsembe yaufa ndi nsembe yothira zalekeka ku nyumba ya Yehova; ansembe, atumiki a Yehova, acita maliro.

10. M'munda mwaonongeka, nthaka ilira; pakuti tirigu waonongeka, vinyo watsopano wamwelera, mafuta akudza pang'onong'ono.

Werengani mutu wathunthu Yoweli 1