Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 9:2-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. anasonkhana kuponyana ndi Yoswa ndi Israyeli, ndi mtima umodzi.

3. Koma pamene nzika za Gibeoni zinamva zimene Yoswa adacitira Yeriko ndi Ai,

4. zinacita momcenierera, nizimuka nizioneka ngati mithenga, nizitenga matumba akale pa aburu ao, ndi matumba a vinyo akale ndi ong'ambika ndi omangamanga;

5. ndi nsapato zakale za zigamba pa mapazi ao, nizibvala nsanza; ndi mikate yonse ya kamba wao inali youma ndi yoyanga nkhungu.

6. Ndipo zinamuka kwa Yoswa kumisasa ku Giligala, niziti kwa iye ndi kwa amuna a Israyeli, Tacokera dziko lakutali, cifukwa cace mupangane nafe.

7. Ndipo amuna a Israyeli anati kwa Ahivi, Kapena mulimkukhala pakati pa ife, ndipo tipanganenji ndi inu?

8. Koma anati kwa Yoswa, Ndife akapolo anu. Pamenepo Yoswa anati kwa iwo, Ndinu ayani? ndipo mufuma kuti

9. Ndipo anati kwa iye, Akapolo anu afumira dziko la kutalitali, cifukwa lea dzina la Yehova Mulungu wanu; pakuti tidamva mbiri yace, ndi zonse anacita m'Aigupto,

10. ndi zonse anacitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya lija la Yordano, Sihoni mfumu ya ku Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya ku Basana wokhala ku Asitorotu.

11. Ndipo akuru athu ndi nzika zonse za m'dziko mwathu zidanena nafe ndi kuti, Mutenge m'dzanja lanu kamba wa paulendo, kakomane naoni, nimunene nao, Ndife akapolo anu; ndipo tsopano mupangane nafe.

12. Mkate wathu uwu tinadzitengera kamba m'nyumba zathu, ukali wamoto, tsiku loturuka Ife kudza kwanu kuno; koma tsopano, taonani, uli wouma ndi woyaoga nkhungu;

13. ndi matumba a vinyo awa tinawadzaza akali atsopano; ndipo taonani, ang'ambika; ndi malaya athu awa ndi nsapato zathu zatha, cifukwa ca ulendo wocokera kutali ndithu.

14. Pamenepo amunawo analandirako kamba wao, osafunsira pakamwa pa Yehova.

15. Ndipo Yoswa anacitirana nao mtendere, napangana nao, akhale amoyo; ndi akalonga a msonkhano anawalumbirira,

16. Ndipo kunali, atatha kupangana nao masiku atatu, anamva kuti ndiwo anansi ao, ndi kuti kwao ndi pakati pao,

Werengani mutu wathunthu Yoswa 9