Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 9:14-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Pamenepo amunawo analandirako kamba wao, osafunsira pakamwa pa Yehova.

15. Ndipo Yoswa anacitirana nao mtendere, napangana nao, akhale amoyo; ndi akalonga a msonkhano anawalumbirira,

16. Ndipo kunali, atatha kupangana nao masiku atatu, anamva kuti ndiwo anansi ao, ndi kuti kwao ndi pakati pao,

17. Ndipo ana a Israyeli anayenda ulendo, nafika ku midzi yap tsiku lacitatu. Koma midzi yao ndiyo Gibeoni, ndi Cefira, ndi Beerotu ndi KiriyatuYearimu.

18. Ndipo ana a Israyeli sanawakantha, pakuti akalonga a msonkhano adawalumbirira kwa Yehova, Mulungu wa Israyeli. Ndipo msonkhano wonse unadandaula pa akalonga,

19. Koma akalonga onse ananena kwa msonkhano wonse, Tinawalumbirira kwa Yehova Mulungu wa Israyeli, m'mwemo sitikhoza kuwacitira kanthu.

20. Tidzawacitira ici, ndi kuwasunga amoyo; ungatigwere mkwiyo cifukwa ca lumbirolo tidawalumbirira.

21. Ndipo akalonga ananena nao, Akhale ndi moyo; ndipo anasanduka akutema nkhuni, ndi otungira madzi msonkhano wonse; monga akalonga adanena nao.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 9