Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 4:3-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. ndipo muwalamulire iwo ndi kuti, Mudzitengere pano pakati pa Yordano, poimapo mapazi a ansembe, miyala khumi ndi iwiri, ndi kuoloka nayo, ndi kulika m'mogona m'mene mugonamo usiku uno.

4. Pamenepo Yoswa anaitana amuna khumi ndi awiriwo amene anawaikiratu mwa ana a Israyeli, pfuko limodzi mwamuna mmodzi;

5. nanena nao Yoswa, Olokani, kutsogolera likasa la Yehova Mulungu wanu pakati pa Yordano, nimudzisenzere yense mwala paphewa pace, monga mwa kuwerenga kwa mapfuko a ana a Israyeli;

6. kuti ici cikhale cizindikilo pakati pa inu. Akakufunsani ana anu m'tsogolomo, ndi kuti, Miyala iyi nja ciani ndi inu?

7. munene nao, Cifukwa madzi a Yordano anadulidwa patsogolo pa likasa la cipangano ca Yehova; muja lidaoloka Yordano, madzi a Yordano anadulidwa; ndipo miyala iyi idzakhala cikumbutso ca ana a Israyeli cikhalire.

8. Ndipo ana a Israyeli anacita monga Yoswa anawalamulira, nasenza miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordano, monga Yehova adalankhula ndi Yoswa, monga mwa kuwerenga kwa mapfuko a ana a Israyeli; ndipo anaoloka nayo kumka kogona, naiika komweko.

9. Ndipo Yoswa anaimika miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordano, poimapo mapazi a ansembe akusenza likasa la cipangano; ikhala komweko kufikira lero lino.

10. Pakuti ansembe akusenza likasa anaima pakati pa Yordano, mpaka zitatha zonse Yehova adazilamulira Yoswa anene kwa anthu, monga mwa zonse Mose adalamulira Yoswa; ndipo anthu anafulumira kuoloka.

11. Ndipo kunali, atatha kuoloka anthu onse, likasa la Yehova linaoloka, ndi ansembe, pamaso pa anthu.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 4