Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 4:20-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndipo Yoswa anaimika ku Giligala miyala ija khumi ndi iwiri adaitenga m'Yordano.

21. Ndipo anati kwa ana a Israyeli, Ana anu akadzafunsa atate ao masiku akudza, ndi kuti, Miyala iyi nja ciani?

22. pamenepo muzidziwitsa ana anu, ndi kuti, Israyeli anaoloka Yordano uyu pouma.

23. Pakuti Yehova Mulungu wanu anaphwetsa madzi a Yordano pamaso panu, mpaka mutaoloka; monga Yehova Mulungu wanu anacitira Nyanja Yofiira, imene anaiphwetsa pamaso pathu, mpaka titaoloka;

24. kuti mitundu yonse ya pa dziko lapansi idziwe dzanja la Yehova, kuti ndilo lamphamvu; kuti lope Yehova Mulungu wanu masiku onse.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 4