Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 3:15-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo pamene iwo akusenza likasa anafika ku Yordano, nathibika m'mphepete mwa madzi mapazi a ansembe akusenza likasa, pakuti Yordano asefuka m'magombe ace onse, nyengo yonse ya masika,

16. pamenepo madzi ocokera kumagwero anaima, nauka ngati mulu, kutalitu ku Adamu, ndiwo mudzi wa ku mbali ya Zaretani; koma madzi akutsikira kumka ku nyanja ya cidikha, ndiyo Nyanja ya Mcere, anadulidwa konse; ndipo anthu anaoloka pandunji pa Yeriko.

17. Ndipo ansembe akulisenza likasa la cipangano la Yehova, anaima pouma pakati pa Yordano, ndi Aisrayeli onse anaoloka pouma mpaka mtundu wonse unatha kuoloka Yordano.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 3