Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 3:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yoswa analawirira mamawa, kucoka ku Sitimu, nafika ku Yordano, iye ndi ana onse a Israyeli; nagona komweko, asanaoloke.

2. Ndipo kunali atapita masiku atatu, akapitao anapita pakati pa cigono;

3. nalamulira anthu, ndi kuti, Mukadzaona likasa la cipangano la Yehova Mulungu wanu, ndi ansembe Aleviwo atalisenza, pamenepo mucoke kwanu ndi kulitsata.

4. Koma pakhale dera pakati pa inu ndi ilo, monga mikono zikwi ziwiri poliyesa; musaliyandikire, kuti mudziwe njira imene muziyendamo; popeza simunapita njirayi kufikira lero.

5. Ndipo Yoswa ananena kwa anthu, Mudzipatule, pakuti mawa Yehova adzacita zodabwiza pakati pa inu.

6. Ndipo Yoswa anati kwa ansembe, Senzani likasa la cipangano, nimuoloke pamaso pa anthu. Nasenza iwo likasa la cipangano, natsogolera anthu.

7. Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero lino ndidzayamba kukukuza pamaso pa Aisrayeli onse, kuti adziwe, kuti monga momwe ndinakhalira ndi Mose, momwemo ndidzakhala ndi iwe.

8. Ndipo uzilamulira ansembe akunyamula likasa la cipangano, ndi kuti, Pamene mufika kumphepete kwa madzi a Yordano muziima m'Yordano.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 3