Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 21:25-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Ndipo motapira pa pfukola Manaselogawika pakati, Taanaki ndi mabusa ace, ndi Gati-rimoni ndi mabusa ace; midzi iwiri.

26. Midzi yonse ya mabanja a ana otsala a Kohati ndiyo khumi ndi mabusa ao.

27. Ndipo anapatsa ana a Gerisoni, a mabanja a Alevi, motapira pa pfuko la Manase logawika pakati, Golani m'Basana ndi mabusa ace, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzaceyo; ndi Beesitera ndi mabusa ace; midzi iwiri.

28. Ndipo motapira pa pfuko la Isakara, Kisioni ndi mabusa ace, Daberati ndi mabusa ace;

29. Yarimutu ndi mabusa ace, Eniganimu ndi mabusa ace; midzi inai.

30. Ndipo motapira pa pfuko La Aseri, Misali ndi mabusa ace, Abidoni ndi mabusa ace;

31. Helikati ndi mabusa ace, ndi Rehobo ndi mabusa ace; midzi inai.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 21