Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 19:1-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo maere aciwiri anamturukira Simeoni, pfuko la ana a Simeoni monga mwa mabanja ao; ndi colowa cao cinali pakati pa colowa ca ana a Yuda.

2. Ndipo anali naco colowa cao Beeri-seba, kapena Seba, ndi Molada;

3. ndi Hazarasuala, ndi Bala, ndi Ezemu;

4. ndi Elitoladi, ndi Betuli, ndi Horimu;

5. ndi Zikilaga, ndi Beti-malikabotu, ndi Hazari-susa:

6. ndi Beti-lebaotu, ndi Saruheni; midzi khumi ndi itatu ndi miraga yao;

7. Aini, Rimoni ndi Eteri ndi Asana; midzi inai ndi miraga yao;

8. ndi miraga yonse yozungulira midzi iyi mpaka Baalata-beeri ndiwo Rama kumwera. Ndico colowa ca pfuko la ana a Simeoni, monga mwa mabanja ao.

9. M'gawo la ana a Yuda muli colowa ca ana a Simeoni; popeza gawo la ana a Yuda linawacurukira; cifukwa cace ana a Simeoni anali naco colowa pakati pa colowa coo.

10. Ndipo maere acitatu anakwecera ana a Zebuloni monga mwa mabanja ao; ndi malire a colowa cao anafikira ku Saridi;

11. nakwera malire ao kumka kumadzulo ndi ku Marala nafikira ku Dabeseti, nafikira ku mtsinje wa patsogolo pa Yokineamu;

12. ndi kucokera ku Saridi anazungulira kumka kum'mawa kumaturukira dzuwa, mpaka malire a Kisilotu-tabori; naturuka kumka ku Daberati, nakwera ku Yafia;

13. ndi pocoka pamenepo anapitirira kumka kum'mawa ku Gati-heferi, ku Etikazini; naturuka ku Remoni umene ulembedwa mpaka ku Nea,

14. nauzungulira malire kumpoto, kumka ku Hanatoni; ndi maturukiro ace anali ku cigwa ca Ifita-eli;

15. ndi Kata, ndi Nahalala ndi Simironi, ndi Idala ndi Betelehemu: midzi khumi ndi iwiri ndi miraga yao.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 19