20. Ndipo malireace mbali ya kum'mawa ndiwo Yordano, ndico colowa ca ana a Benjamini, kunena za malire ace pozungulira pace, monga mwa mabanja ao.
21. Koma midzi ya pfuko la ana a Benjamini monga mwa mabanja ao ndiyo Yeriko, ndi Beti-hogila, ndi Emekikozizi;
22. ndi Beti-araba, ndi Zemaraimu, ndi Beteli;
23. ndi Arimu ndi Para, ndi Ofira;
24. ndi Kefaraamoni, ndi Ofini, ndi Geba; midzi khumi ndi iwiri pamodzi ndi miraga yao;
25. Gibeoni ndi Rama, ndi Beeroti;
26. ndi Mizipe, ndi Kefira, ndi Moza;
27. ndi Rekemu, ndi Iripeeli ndi Tarala;