Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 18:10-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo Yoswa anawalotera maere ku Silo pamaso pa Yehova; ndi apo Yoswa anawagawira ana a Israyeli dziko, monga mwa magawo ao.

11. Ndipo maere a ana a Benjamini anakwera monga mwa mabanja ao; ndi malire a gawo lao anaturuka pakati pa ana a Yuda ndi ana a Yosefe.

12. Ndipo malire ao a kumpoto anacokera ku Yordano; ndi malire anakwera ku mbali ya Yeriko kumpoto, nakwera pakati pa mapiri kumadzulo; ndi maturukiro ace anali ku cipululu ca Beti-aveni.

13. Ndipo malire anapitirirapo kumka ku Luzi, ku mbali ya Luzi, momwemo ndi Beteli, kumwela; ndi malire anatsikira kumka ku Atarotu-adara, ku phiri lokhala kumwela kwa Betihoroni wa kunsi.

14. Ndipo malire analembedwa nazungulira ku mbali ya kumadzulo kumka kumwela, kucokera ku phiri pokhala patsogolo pa Beti-horoni, kumwela kwace; ndi maturukiro ace anali ku Kiriyatibaala, womwewo ndi Kiriyati-Yearimu, mudzi wa ana a Yuda; ndiyo mbali ya kumadzulo.

15. Ndipo mbali ya kumwela inayambira polekezera Kiriyati-Yearimu; naturuka malire kumka kumadzulo, naturuka kumka ku citsime ca madzi a Nefitoa;

16. natsikira malire kumka polekezera phiri lokhala patsogolo pa cigwa ca mwana wa Hinomu, ndico ca m'cigwa ca Refai kumpoto; natsikira ku cigwa ca Hinomu, ku mbali ya Ayebusi kumwela, natsikira ku Enirogeli;

17. nalembedwa kumka kumpoto, naturuka ku Eni-semesi, naturuka ku Gelilotu, ndiwo pandunji pokwerera pa Adumi; natsikira ku mwala wa Bohani mwana wa Rubeni;

18. napitirira ku mbali ya pandunji pa Araba kumpoto, natsikira kumka ku Araba;

19. napitirira malire kumka ku mbali ya Beti-hogila kumpoto; ndi maturukiro ace a malire anali ku nyondo ya kumpoto ya Nyanja ya Mcere; pa kulekezera kwa kumwela kwa Yordano; ndiwo malire a kumwera.

20. Ndipo malireace mbali ya kum'mawa ndiwo Yordano, ndico colowa ca ana a Benjamini, kunena za malire ace pozungulira pace, monga mwa mabanja ao.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 18