Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 10:9-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo Yoswa anawadzidzimukitsa; popeza anakwera kucokera ku Giligala usiku wonse.

10. Ndipo Yehova anawamwaza pamaso pa Israyeli, ndipo anawakantha makanthidwe akuru ku Gibeoni, nawapitikitsa pa njira yokwera ya Betihoroni, nawakantha mpaka Azeka, ndi mpaka Makeda.

11. Ndipo kunali, pakuthawa iwo pamaso pa Israyeli, potsikira pa Betihoroni, Yehova anawagwetsera miyala yaikuru yocokera kumwamba mpaka pa Azeka, nafa iwo; akufa ndi miyala yamatalala anacuruka ndi iwo amene ana a Israyeli anawapha ndi lupanga.

12. Pomwepo Yoswa ananena kwa Yehova tsiku limene Yehova anapereka Aamori pamaso pa ana a Israyeli; ndipo anati pamaso pa Israyeli,Dzuwa iwe, linda, pa Gibeoni,Ndi Mwezi iwe, m'cigwa ca Aialo.

13. Ndipo dzuwa linalinda, ndi mwezi unaimaMpaka anthu adabwezera cilango adani ao.Kodi ici sicilembedwa m'buku la Yasari? Ndipo dzuwa linakhala pakati pa thambo, losafulumira kulowa ngati tsiku lamphumphu.

14. Ndipo panalibe tsiku lotere kale lonse kapena m'tsogolomo, lakuti Yehova anamvera mau a munthu; pakuti Yehova anathirira Israyeli nkhondo.

15. Pamenepo Yoswa anabwerera, ndi Aisrayeli onse pamodzi naye, ku cigono ca ku Giligala.

16. Ndipo mafumu awa asanu anathawa, nabisala m'phanga la ku Makeda,

17. Ndipo anauza Yoswa ndi kuti, Mafumu asanuwa apezeka obisala m'phanga la ku Makeda.

18. Ndipo Yoswa anati, Kunkhunizirani miyala yaikuru kukamwa kwa phanga, ndi kuikapo anthu, awasunge;

19. koma inu musaime, pitikitsani adani anu, ndi kukantha a m'mbuyo mwao; musawalole alowe m'midzi mwao; pakuti Yehova Mulungu wanu anawapereka m'dzanja lanu.

20. Ndipo kunali, Yoswa ndi ana a Israyeli atatha kuwakantha, makanthidwe akurukuru mpaka atatha psiti, ndipo otsala a iwo atalowa m'midzi ya malinga,

21. anthu onse anabwerera kucigono kwa Yoswa pa Makeda ndi mtendere. Palibe munthu anacitira cipongwe mmodzi yense wa ana a Israyeli.

22. Pamenepo Yoswa anati, Tsegula pakamwa pa phanga ndi kunditurutsira m'phanga mafumu asanuwo.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 10