Ndipo kunali, pakuthawa iwo pamaso pa Israyeli, potsikira pa Betihoroni, Yehova anawagwetsera miyala yaikuru yocokera kumwamba mpaka pa Azeka, nafa iwo; akufa ndi miyala yamatalala anacuruka ndi iwo amene ana a Israyeli anawapha ndi lupanga.