Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 10:3-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Cifukwa cace Adoni-Zedeki anatuma kwa Hohamu, mfumu ya Hebroni, ndi kwa Piraniu mfumu ya Yarimutu, ndi kwa Yafiya mfumu ya Lakisi, ndi kwa Dibri mfumu va Egiloni, ndi kuti,

4. Kwerani kwanga kuno, ndi kundithandiza kuti tikanthe Gibeoni, pakuti unacitirana mtendere ndi Yoswa ndi ana a Israyeli.

5. Pamenepo mafumu asanu a Aamori, ndiwo mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yarimutu, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni anasonkhana, nakwera iwo ndi makamu ao onse namanga misasa pa Gibeoni, nauthira nkhondo.

6. Ndipo amuna a ku Gibeoni anatumira Yoswa mau kucigono ku Giligala, ndi kuti, Musalekerere akapolo anu; mutikwerere msanga, ndi kutipulumutsa, ndi kutithandiza; pakuti mafumu onse a Aamori, akukhala kumapiri atisonkhanira.

7. Pamenepo Yoswa anakwera kucokera ku Giligala, iye ndi anthu onse a nkhondo pamodzi naye, ndi ngwazi yose.

8. Ndipo Yehova ananena ndi Yoswa, Usawaope, pakuti ndawapereka m'dzanja lako; palibe mmodzi wa iwo adzaima pamaso pako.

9. Ndipo Yoswa anawadzidzimukitsa; popeza anakwera kucokera ku Giligala usiku wonse.

10. Ndipo Yehova anawamwaza pamaso pa Israyeli, ndipo anawakantha makanthidwe akuru ku Gibeoni, nawapitikitsa pa njira yokwera ya Betihoroni, nawakantha mpaka Azeka, ndi mpaka Makeda.

11. Ndipo kunali, pakuthawa iwo pamaso pa Israyeli, potsikira pa Betihoroni, Yehova anawagwetsera miyala yaikuru yocokera kumwamba mpaka pa Azeka, nafa iwo; akufa ndi miyala yamatalala anacuruka ndi iwo amene ana a Israyeli anawapha ndi lupanga.

12. Pomwepo Yoswa ananena kwa Yehova tsiku limene Yehova anapereka Aamori pamaso pa ana a Israyeli; ndipo anati pamaso pa Israyeli,Dzuwa iwe, linda, pa Gibeoni,Ndi Mwezi iwe, m'cigwa ca Aialo.

13. Ndipo dzuwa linalinda, ndi mwezi unaimaMpaka anthu adabwezera cilango adani ao.Kodi ici sicilembedwa m'buku la Yasari? Ndipo dzuwa linakhala pakati pa thambo, losafulumira kulowa ngati tsiku lamphumphu.

14. Ndipo panalibe tsiku lotere kale lonse kapena m'tsogolomo, lakuti Yehova anamvera mau a munthu; pakuti Yehova anathirira Israyeli nkhondo.

15. Pamenepo Yoswa anabwerera, ndi Aisrayeli onse pamodzi naye, ku cigono ca ku Giligala.

16. Ndipo mafumu awa asanu anathawa, nabisala m'phanga la ku Makeda,

17. Ndipo anauza Yoswa ndi kuti, Mafumu asanuwa apezeka obisala m'phanga la ku Makeda.

18. Ndipo Yoswa anati, Kunkhunizirani miyala yaikuru kukamwa kwa phanga, ndi kuikapo anthu, awasunge;

19. koma inu musaime, pitikitsani adani anu, ndi kukantha a m'mbuyo mwao; musawalole alowe m'midzi mwao; pakuti Yehova Mulungu wanu anawapereka m'dzanja lanu.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 10