16. Ndipo anamyankha Yoswa, nati, Zonse mwatilamulira tidzacita, ndipo kuli konse mutitumako tidzamuka.
17. Monga momwe tinamvera mau onse a Mose momwemo tidzamvera inu; komatu akhale ndi inu Yehova Mulungu wanu monga anakhala ndi Mose.
18. Ali yense wakupikisana ndi inu, osamvera mau anu muli monse mukamlamulira, aphedwe; komatu khalani wamphamvu, nimulimbike mtima.