Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yona 4:2-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo anapemphera kwa Yehova, nati, Ha, Yehova! si ndiwo mau anga ndikali m'dziko langa? cifukwa cace ndinafulumira kuthawira ku Tarisi, pakuti ndinadziwa kuti Inu ndinu Mulungu wacisomo ndi wodzala cifundo, wolekerera ndi wokoma mtima mocuruka, ndi woleka coipaco.

3. Ndipo tsopano, Yehova, mundicotseretu moyo wanga, kundikomera ine kufa, osakhala ndi moyo ai.

4. Ndipo Yehova anati, Uyenera kupsa mtima kodi?

5. Pamenepo Yona anaturuka m'mudzi, nakhala pansi kum'mawa kwa mudzi, nadzimangira komweko thandala, nakhala pansi pace mumthunzi mpaka adzaona cocitikira mudzi.

6. Ndipo Yehova Mulungu anaikiratu msatsi, naumeretsera Yona, ucite mthunzi pamutu pace, kumlanditsa m'nsautso yace. Ndipo Yona anakondwera kwambiri cifukwa ca msatsiwo.

Werengani mutu wathunthu Yona 4