Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yona 3:5-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo anthu a Nineve anakhulupirira Mulungu, nalalikira cosala, nabvala ciguduli, kuyambira wamkuru kufikira wamng'ono wa iwowa.

6. Pakuti mau awa anafikira mfumu ya Nineve, ndipo Inanyamuka ku mpando wace wacifumu, nibvula copfunda cace, nipfunda ciguduli, nikhala m'mapulusa.

7. Ndipo analalikira, nanena m'Nineve mwa lamulo la mfumu ndi nduna zace, ndi kuti, Ngakhale munthu kapena nyama, ngakhale ng'ombe kapena nkhosa, zisalawe kanthu, zisadye, zisamwe madzi;

Werengani mutu wathunthu Yona 3