Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yona 3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Yona ku Nineve, Kulapa kwa a ku Nineve

1. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yona nthawi yaciwiri, ndi kuti,

2. Nyamuka, pita ku Nineve mudzi waukuru uja, nuulalikire uthenga umene ndikuuza.

3. Ndipo Yona ananyamuka, napita ku Nineve, monga mwa mau a Yehova. Koma Nineve ndiwo mudzi waukuru pamaso pa Yehova, wa ulendo wa masiku atatu.

4. Ndipo Yona anayamba kulowa mudziwo ulendo wa tsiku limodzi, nalalikira, nati, Atsala masiku makumi anai ndipo Nineve adzapasuka.

5. Ndipo anthu a Nineve anakhulupirira Mulungu, nalalikira cosala, nabvala ciguduli, kuyambira wamkuru kufikira wamng'ono wa iwowa.

6. Pakuti mau awa anafikira mfumu ya Nineve, ndipo Inanyamuka ku mpando wace wacifumu, nibvula copfunda cace, nipfunda ciguduli, nikhala m'mapulusa.

7. Ndipo analalikira, nanena m'Nineve mwa lamulo la mfumu ndi nduna zace, ndi kuti, Ngakhale munthu kapena nyama, ngakhale ng'ombe kapena nkhosa, zisalawe kanthu, zisadye, zisamwe madzi;

8. koma zipfundidwe ndi ciguduli munthu ndi nyama, nizipfuulire kolimba kwa Mulungu; ndipo abwere yense kuleka njira yace yoipa, ndi ciwawa ciri m'manja mwace.

9. Kaya, akatembenuka Mulungu, ndi kuleka kubwera ku mkwiyo wace waukali, kuti tisatayike,

10. Ndipo Mulungu anaona nchito zao, kuti anabwera kuleka njira yao yoipa; ndipo Mulungu analeka coipa adanenaci kuti adzawacitira, osacicita.