Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yona 2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Pemphero la Yona ali m'mimba mwa cinsomba

1. Pamenepo Yona anapemphera kwa Yehova Mulungu wace ali m'mimba mwa nsombayo.

2. Ndipo anati,Ndinaitana Yehova m'nsautso yanga,Ndipo anandiyankha ine;Ndinapfuula ndiri m'mimba ya manda,Ndipo munamva mau anga.

3. Pakuti munandiponya mwakuya m'kati mwa nyanja,Ndipo madzi anandizinga;Mapfunde anu onse a nyondonyondo anandimiza.

4. Ndipo ndinati, Ndatayika ndicoke pamaso panu;Koma ndidzapenyanso Kacisi wanu wopatulika.

5. Madzi anandizinga mpaka moyo wanga,Madzi akuya anandizungulira,Kayandeyande wa m'nyanja anandikulunga mutu.

6. Ndinatsikira ku matsinde a mapiri,Mipingiridzo ya dziko inanditsekereza kosatha;Koma munandikwezera moyo wanga kuucotsa kucionongeko, Yehova Mulungu wanga.

7. Pokomoka moyo wanga m'kati mwanga ndinakumbukila Yehova;Ndi pemphero langa linafikira Inu m'Kacisi wanu wopatulika.

8. Iwo osamalira mabodza opanda paceAtaya cifundo cao cao.

9. Koma ine ndidzakupherani Inu nsembe ndi mau akuyamika,Ndidzakwaniritsacowindacanga.Cipulumutso nca Yehova.

10. Pamenepo Yehova analankhula ndi nsombayo, ndipo inamsanzira Yona kumtunda.