Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yona 1:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. NDIPO mau a Yehova anadza kwa Yona mwana wa Amitai, ndi kuti,

2. Nyamuka, pita ku Nineve, mudzi waukuruwo, nulalikire motsutsana nao; pakuti coipa cao candikwerera pamaso panga.

3. Koma Yona ananyamuka kuti athawire ku Tarisi, kuzemba Yehova; ndipo anatsikira ku Yopa, napezako combo comuka ku Tarisi, napereka ndalama zace, natsikira m'menemo, kuti apite nao ku Tarisi kuzemba Yehova.

4. Koma Yehova anautsa cimphepo cacikuru panyanja, ndipo panali namondwe wamkuru panyanja, ndi combo cikadasweka.

5. Pamenepo amarinyero anacita mantha, napfuulira yense kwa mlungu wace, naponya m'nyanja akatundu anali m'combo kucipepuza. Koma Yona adatsikira m'munsi mwa combo, nagona tulo tofa nato.

6. Ndipo mwini combo anadza kwa iye, nanena naye, Utani iwe wam'tulo? uka, itana Mulungu wako, kapena Mulunguyo adzatikumbukila tingatayike.

Werengani mutu wathunthu Yona 1